[Lyrics]Mr Praise – Nthawi ft SayNewz

 [Lyrics]Mr Praise – Nthawi ft SayNewz

Nthawi by Mr Praise & SayNewz Lyrics

Verse 1

Palibe olo mmozi akudziwa tsikulo/
Kuti uzakhala Masana kapenanso madzulo/
Kudabwa mzako wapita umacheza naye dzulo/
Kukanika kumvetsa ngati zachitika mtulo/
Ndiye mmene zinalili mmatsiku a Noah/
Ndimeneso zilili matsiku anowa/
Ma plans aukwati ali mkati mophikidwa/
Mmalo mokwatilana mmoziyo nkukwatulidwa/
Ma signs aonetsa nthawi yayandikira/
Mtundu kuukirana, njala komanso nthenda/
Kupanga legalise zomwe zili zoipa..mau ananena kale pano zikuchitika/
Nthawi ikuyenda ndipo ili close/
Kutembenuka mtima si tomorrow of course/
Nthawi ndi yomweyi mulandire upulumuke/
Mmanja mwake ukhala safe sangalore upulumuke

Chorus
Kudzakhala chimwemwe kwa onse oyera mtima/
Kudzakhala chimwemwe kwa onse oyera mtima/
Adzawonana ndi Mbuye wao/
Adzawonana, ndi Mbuye Yesuu!

Verse 2
Sakubwera Ngati mwana ayi akubwera ndi Glory/
Sakubwera kuzakhala kma kuti azakolore/
Anabwera kale kuti ochimwa onse apulumuke/
But this time akubwera olungama tinyamuke/
Zili ngati mayeso ofunika kukonzekera/
Kuyamba study tsiku lomwelo sizikuyendera/
Iwe nzotheka kupulumuka osaziyeza taya ruler/
Look at us talandira yesu mphasa tayalura /
Tidzasangalala heavy ndi maso kuzamupenya/ Tidzamuona reality osatiso masomphenya/
Ndiye ndifunse kodi inu mumakhalira ndani/
Ntambasule kodi moyo wanu mwini wake ndi ndani?/
Yesu ndiye wosunga moyo tsegula mtima nku surrender/
Kumwamba ndikokoma yemwe amafuna azasale nda?

Chorus
Kudzakhala chimwemwe kwa onse oyera mtima/
Kudzakhala chimwemwe kwa onse oyera mtima/
Adzawonana ndi Mbuye wao/
Adzawonana, ndi Mbuye Yesuu!

Verse 3

Kodi m’bale wakonzeka?

Kulandira Moyo/
Kodi M’bale wakonzeka?
Kukumana naye/
Yesu akubwera, posachedwa/
Mfumu ikubweraa, posachedwa/
Hallelujah!

Back to chorus