BlessMe Drops Chilembwe Tribute: Nkhwangwa Pa Mwala

 BlessMe Drops Chilembwe Tribute: Nkhwangwa Pa Mwala

Title: Nkhwangwa pa Mwala
Artist: Blessme
Producers: Inkosi Music, Hope CZ

Verse 1

Gwero la umphawi wathu ndinu nomwe
Mudatitenga ukapolo nkunka nafe komwe
Kusiyana ana ndi amayi awo kuno akulira
Pamudzi popanda mphongo ndipo akulira
Munagawa malire pa nthaka yathu
Mosalingalira kaye za mitundu yathu
Lero tikungophana, mudatigawanitsa
Nde mwabweranso mudzina lodzatiyanjanitsa
Abodza inu, nkhondo zathu ndi ntanji wanu
Kumatibela golide pomwe tikumenyana
Zomwe mumafuna, tizingokupemphani
Nde tizikuopani, nkumakupembedzani
Kutikakamiza, makhalidwe onyasa
Nkumati apo bii, thandizo lanu tigasa
Mtima chodzikomda, chintima cha nkhaza
Olo mutikakamize here is the answer

Hook

Tatementsa nkhwangwa pa mwala (x4)

Verse 2

Takana kusinthanitsa umunthu ndi nsima
Nfunseni G-Newo, uwo ndi ukwati wamumdima
Mufunseni Chiwamba, tonse takana matha
Mxieew olo mutiopseze tiribe mantha….
Mwanenepa potidyera masuku pamutu
Nkumaima pa chulu, kuyankhula za mkutu
Kumati ndife aulesi, opada nzeru
No wonder, Chilembwe anachita nalo nseru
Khalidwe lanu loipa la nkhaza, thangata
Anakuukirani eeh eh nanga akanata?
Uwuse muntendere mzimu wake ndi wa Idah
inunso ndi akhanza chimodzimodzi Al Qaeda
Tasankha kuyanjana sumungatigwetse
Pa nthaka yathu tilimapo, simungatiletse
Ndipo ufulu wathu sitingaubetse
Sitiloranso kuti mwazi wathu muukhetse

Back to Hook

Blessme – Nkhwangwa Pa Mwala (prod Inkosi Music & Hope CZ)